BVUMBULUTSO LA BUKU LA AROMA
UTHEGA OBISIKA WA PAULO.
OLEMBEDWA KUCHOKERA M’MABUKU
OYAMBILIRA NDI FRANCOIS du TOIT.
Translated by Brother Lawrence of the Ats Pentecostal Church, Blantyre
MAWU OYAMBA
CHIOMBA NKHANGA CHA UFULU
Paulendo omwe ine ndi mkazi wanga Lydia tinapita kukasangalala titandokwatisa kumene ukwati wathu mu January 1779, tinapita ku Blydepoort, ku mpumalanga. Tinakumana ndi oyan’ganira nkhalango yemwe anatiuza za momwe anachitira nawo mwambo otulusa Chiomba nkhnga m’chikwele momwe chinasungidwamo kwa zaka khumi, ku malo osungilamo nyama(zoo) ku Pretoria.
Anatiuza kuti kunali chimwemwe ndi chiyembekezo pamene anali kuyembekezera kutsengula khomo la chikwere kuchipatsa chiombakhanga ufulu wake.
Koma zinali zosiyana kutulutsa chiombankhanga m’chikwere ndi kuchosa chikwere m’maganizo a chiombakhanga.
Maganizo anali muundende m’chikwere ku Pretoria.
Aliyense anagwira pakamwa kuona mbalame yomwe ndi ya mphamvu ili mu umphawi ndi undende oziyan’ganila pansi.
Palibe chomwe chinasitha kwa chiombakhangacho mpaka pomwe chinamva chiombankhnga china chomwe chinanali muufulu chikulira m’wamba. Maso a chiombankhanga chozolowera m’chikwerechi anatseguka ndipo chinauluka kupita mlengalenga ngati kale. Sichinasowekelenso kuphunzira kuuluka.
Nkhani yopatsa chidwiyi inandikhudza kwambiri.Ndinazindikira kuti m’mabvumbulutso authenga wa bwino wa Paolo muli chifunika chimodzi ndicho kulalikira ku mafuko ndi kulimbika mtima za choonadi chwnicheni chomwe munthu ali, komanso ugwiro ndi kupanda kutsutsika kwale kwa munthu.
UTHENGA WA PAULO.
Mu kalata yake ku Aroma, Paulo akulemekeza uthenga wa bwino wa Yesu khristu mosiyana ndi ena. Mukawelenga kalata yofunikayi m’buku lopatulika, mumvetsa chifukwachake Paulo akuyankhula mwa mphavu za uthenga wabwino. Akuchiteslatu chinyengo chilichitse choti wina sangaonjezere kapena kuchotesra pa mabvumbulutso amenewa. Zikukhudza munthu yense: momwemulengi anakwaenilitsira kuombola ndi kubwezeletsera chifanizo chake mumaonekedwe a munthu.
Paulo akuonetsera kuti zonse zimene zinachitika ku mtundu wa munthu chifukaw cha ku chimwa kwa Adamu, zinabwezeletesdwa mwa munthu kupyolera mu bvumbulutso lakuti moyo wa munthuunali nawo mu imfa, ndi kuukitsidwa kwa Yesu khristu.
Akuonetsera kuti kuchimwa kwa Adamu ndi kuchita konse kosalungama kunagonjetsedwa ndi ndi chilungamo cha Mulungu mwa Yesu khristru kuchitsa mlandu wa machismo kwa munthu. Malamulo onse amene munthu angatsate kapena kuchita khama ndi mphamvu zake kuti akhale olungam,kuzidzoloweletsa kuchita bwino zimapanga ntchito yomwe Yesu anagwira kukhala ngati yopanda pake. “chotupitsa pan’gono chitupitsa mtanda wonse” anatero mukalata wake kwa Agalatiya(5:5)
Bvumbulutso la chilungamo mwa chikhulupiliro limaonetsa momwe Mulungu mwa khristu anapambanila kubweletsa munthu mu chimene anali pa chiyambi asanachimwe.
Tanthauzo lenileni la mawu oti “chilungamo” ndiko kuti mbali ziwirizilindi zofanana mwa winandi mzake, popanda kutonzana, kutsutsika kapena kudelelana.
Mulalata yake Paulo akuonetselatu kuti sanabweleke mawu, kapena mabvumbulutso, kuchokera ku mabuku ena kapena kwa Atumwi khumi ndi m’modzi omwe anayenda ndi Yesu. “pakutindiku ziwisani inu abale za uthenga wabwino wolalikidwa ndi ine kuti suli monga mwa munthu, kapena sindinauphunzira komatu unadza mwa bvumbulutso la Yesu khristu.”
Pakuti munamva za makhalidwe anga kale mwa chiyuda, kuti ndinalondalonda mpingo wa Mulungu koposa ndi kuupasula. Ndipo ndinakghala wachangu koposa pa miyambo ya makolo anga.
Koma pamene panakondweretsaMulungu, amene mwana wake mwa ife, kuti ndimulalikire iye mwa Amitundu; pomwepo sindifunsana ndi thupi ndi mwazi(Agal 1:11, 12, 15-17)
Mwina tikhoza kunena kuti Paulo anataya mwayi waukulu kuti momwe anatembenuka sanapite kwa Atumwi omwe anayenda ndi Yesu kuit anamufotokodzere mbiri yonse ya Yesu wa ku Nazareti.
Koma mphamvu yakukumana ndi Yesu inamupangitsa kuti asadziwelengere yekha mumbiri ya kubadwa kwake. Zopindula zonse anali nazo monga obadwa mwa fuko la Benjamini zikhala chabe chifukwa cha bvumbulutso la uzimu la chomwe munthu ali.
“Kotero ife sitiziwanso munthu tsopano monga mwa thupi......(2Akolinto 5:16)”
“Palibe myuda muno kapena mhelene, mulibe kapolo kapena mfulu,mulibe wamkadzi kapena wa m’muna”(gal 3:28)
Palibe chomwe chimasiyanitsa munthu koposa bvumbulutso la chiomene naali pachiyambi, mwa khristu. Mwa khristu chifanizo ndi chikhalidwe cha Mulungu osaoneka chinaonekelanso mwa munthu. “pakujti mwa iye chikhala chidzalo cha umulungu m’thipi, ndipo muli odzadzidwa mwa iye”……(Akolose 2:9-10)
“Ngakhale sakhala patali ndi modzi wa ife”, Paulo akuchenjenza ophunzira,anzeru aku Atene, pakuti mwa iye tikhala ndi moyo ndi kuyendayenda ndi kupeza m’khalidwe wathu; pakuti tili mbadwa zake”…..(machitidwe 17:27,28). Kalilole wake wa wa mkati akuphera mphongo! Chikhalidwe chathu monga Yesu chabvumbulisidwa mwa ife chimabweletsa kusinthika. Kuzindikira ichi nkoposa maganizo ndi zofuna zathu.(2Akolinto 3:18). Ngakhale nkomodzi komwe, Paulo sanatchulepo zazozizwa zomwe Yesu anachita kapena kapena kulakhulapo za mafanizo mumakalata ake.
Ntchito ndi cholinga chake sichinali ku bvumbulutsa khristu mu mbiri koma kubvumbulutsa khristu mwa ife! (Aroma8:10) Anasangalala za zokolola zobvumbulusidwa mu mbewu ya tilingu imene ikanakhala yokha, ikanati sinafetsedwe m’dothi ndi kufa. (Yohane12:23,24).
Chinsinsi chomwe chinabisika kumibadwo ya Anthu, chimene ailamuliro a pa dziko lino sanachimvetse. Mulungu anasunga chinsinsi chimenechi mwa kubadwe kwa khristu kuti munthu alemekezedwe. Akanadziwa chimenechi sakana pachika Yesu pa mtanda(1 akolinto 2:6-9)
Koma sanamvetse chinsinsi cha cholinga cha Mulungu m’mene munthu anapedzekera mwa khristu, m’mene m’modzi anafera onse, ndi m’menenso onse nanfera nawo mu imfa yake.(2Akolinto 5:14). Sanazindikire mmene anthu adzapulumikira munyengo imodzi chifukwa cha munthu m’modzi, ndikulanda ulamuliro wa m’dima ndi umbuli pa anthu onse. “masiku akusaziwa Mulungu analekelera”(machitidwe17:30)
Mbiri ya kufa ndi kuuka kwa munthu m’modzi inalembedwa, kumwamba kunalembedwa kufa kwa mtundu onse ndi kubadwa kwa mtundu wa anthu. Mukusadziwa kwathu takhala tikumukuza m’dyelekezi, chikhalilecho ali ogonjetsedwa! Mubvumbulutso la uthenga wa bwino ankhalisidwa chete ndipo ndi opanda mphamvu!(2 Akolinto 2:6-8, Akolose2:14,15).
Chilinga chake ndicho kumpanga munthu kukhala mbuli kuti asadziwe chomwe ali mwa khristu monga iye. Kusadziwa ndi kusakhulupira kwathu kumapatsa iye mphamvu.
M’chipagano chonse chakale, ndipamodzi pokha tikuwelenga za kuuka kwa akufa tsiku lachitatu kuti ziktikhudza ife! “tsiku lachitatu adzatiutsa!” (hoseya1:2) Awa ndi mawu ndi mawu omwe adpeka kumvetsa kwa Paulo kuti tonse tinalinawo mu imfa ndi kuukitsidwa kwa Yesu. Kodi tinayenera bwanji?
“Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu” Anatero Paulo pa 2Akolinto 5:18 “Koma kwa iye muli inu mwa khristu Yesu” (1Akolinto1;31) Iwo azadza nadzafotokozera chilungamo chake kwa anthu akadzabadwa kuti iye anachita.(masalimo22:31) Izi zinachitika m’malo mwathu ife tikanali m’machimo(Afilipi 2:5,6) Chifukwa tinauka naye limodzi Yesu. Tiyeni tsopano tidzadze malingaliro athu ndi m’nchipinda cha ulamuliro, osadzatsutsanso tokha ndi mayendedwe a moyo wa wamba(Akolose 3:1-3)
Paulo anapita ku Yerusalemu kwa masabata awiri atakhala zaka zitatu ku Arabiya payekha.Ali ku Jerusalemu, anangokumanako ndi Atumwi awiri okha, waa ndi Kephasi ndi Yakobo,m’bale wake wa Yesu. Ndi chiyani chomwe chinasiyanitsa Atumwi awiriwa kuti Paulo asakhe kukumana nawo? Atumwi amenewa anali ndi mabvumbulutso ofanana ndi Paulo; sanamuziwe Yesu monga munthu chabe; anazindikira chimenew iwo anali mwa khristu.
Paulo anamutcha Petulo, Kephasi mwadala ndi cholinga choonetsa tathauzo la dzina mu chinenelo chomwe chipangano chatsopano chinalembedwera; m’chigiliki, mawu akuti “Petros” atanthauza “thanthwe” Koma mu chiyankhulo cha Aramiki thanthwe ndi Kephasi.
Pa mateyu 16 Yesu anafutsa funso lofunika kwambiri m’buku lonse lopatulika. ‘Kodi anthu amati mwana wa munthu ndani?” mwa bvumbulutso Simoni anaonetsa kuti Yesu si mwana wa Yosefe, koma Mesiya. Iyeyu ndiye lonjezano la chipulumutso, chifaniziro ndi chikhalidwe cha mulungu chimene chinabweletsedwa ndi kuonetseledwa mu thupi la munthu, mwana wa Mulungu wa moyo.
Taonani m’mene Yesu anayankhira Simon; odala iwe Simon mwana wa Yona, popeza thupi ndi mwazi sizinakuululira chimenechi koma Atate wanga ndiwo. Ngati ine ndili mwana wa Mulungu inunso muli! Dzina lako silili lochokera kwa Bambo ako a thupi koma kuchokera m’thanthwe lomwe linabala iwe(Deuteronomo 32:18) “mwaleka thanthwe limene linakubalani”.(Yesaya 51:1) Pathanthwe limeneri ndizamanga mpingo wanga.
Mawu akuti “Church” muchingelezi anachokera ku chi Griki “ekklesia”. Mpingo ndilo yakho kwa munthu yemwe anatata chikhalidwe chake.Mawu okuti Ekklesia amene Yesu ananena, sayankhula za nyumba yopepheralamo kapena bungwe koma naatathauza chikhalidwe chenicheni chimene munthu ali ndipo chinabvumbulutsidwa ndi kubwedzeletsedwa mwa khristu monga kalilole. Mawu oyamba akuti Ekklesia, EK, amayakhula za ugwiro kapena pandunji pomwe panayambira kathu.(1 Akorinto 1:30, Ahebri2:11) ndipo klesia, akuchokera ku mawu akuti kaleo, kutathauza kuzindilidwa ndi dzina la Mtundu wako, Atate wako.
Tanthauzo ndi cholinga cha mpingo ndicho kupitiliza utumiki wa Yesu khristu umene ndikuzindikilitsa anthu kuti mwa ife muli maonekedwe a Yesu khristu “Anatibalanso ku chiyembekezo cha moyo wakuuka kwa kufa kufikila kwa Yesu khristu”(1petro1:3)
Kodi ndi chifukwa chiyani Paulo anakumananso ndi Yakobo pamodzi ndi Petulo?(agalatiya1:19) Kodi chinachitika ndi chiyani kuti Yakobo asatenge nao mbali pa utumiki wa m’bale Yesu? (Pakuti angakhale abale ake sanankhulupirire iye) (Yohane7:5) chinampangitsa ndi chiyani kuti anene kuti tinabadwa mwa Atate wa kuunika, yemwe anatibala ndi mawu a choonadi?
Chiyambi chathu choona chili mwa Mulungu; ife ndife ntchito ya manja ake, ndipo “Pakuti ngati munthu ali wa kumva mau, aona nkhope yake monga pakalilole. Komanso akuti mkotheka kuiwala m’mene nkhope yako ionekela ngati wataya chikhulupirilo cha momwe unalili pakalilole ndi kubwelera monga munthu wa malingalilo awiri(yakobo1:17,18, 24 )
Pa 1 Akolinto 15:7 Paulo akuyankhulanso kuti Yesu anaonekera kwa Yakobo atauka kwa akufa. Ndikhulupilira kuti apa mpomwe analandirapo utumiki wa Yesu. Tsopano wazindikira kuti m’bale wake analidi Mesiya, komanso wazindikira kuti monga Yesu, nayenso anabadwa mwa Mulungu; komanso anthu onse anabadwa mwa Mulungu, Yosefe ndi Maliya sanali makolo a moyo wawo mwa mzimu.
Paulo watsimikiza kuti china chake chachitika kwa munthu mu imfa ndi kuuka kwa Yesu khristu. Chiukitso ndicho chimene chionetsera kubadwa kwa tsopano. Ichi chinachitika angakhale ife tisakuzindikira. “Ngakhale tinali akufa mu zolakwa zathu anatipatsa moyo pamodzi ndi Khristu”(Aefeso 2:5) pamene Paulo analalikira za chiukitso ku machitidwe Atumwi 13 anagwiritsa ntchito masalimo 2, “ine lero ndakubala”(Machitindwe 13:30-33)
“Pakuti monga mwa Adamu onse amwalira, choteronso mwa khristu onse akhalitsidwa ndi moyo” (1Akolinto 15:22) Yesu sanali wapambuyo koma Adamu omaliza. Zithu zakale za Adamu) zapita “ munthu oyamba Adamu anakhala mzimu wa moyo,Adamu wotsilizayo anakhala mzimu wakulenga moyo” (1Akolinto 15:45) “popeza taweza chotero kuti m’modzi anafera onse n’chifukwa chake onse anafa; kotero kuti ife sitidziwanso munthu tsopano monga mwa thupi: mwa khristu munthu ndi olengedwanso mwa tsopano. Zakale zapita taonani zakhala za tsopano”(2 Akolinto 5:14,16,17)
Kodi anthu onse nafa liti? Mu chiphunzinso cha Paulo izi zinachitika pamene Yesu anafa. Yesu mu umunthu wake anaimilira Mulungu mu thupi ndi mtundu onse wa anthu.Yesu sanabwele kuzayamba chipembenzo chatsopano; anabwera kudzabvumbulutsa chikhalidwe cheni cheni cha munthu ndi kukhululukidwa ku Agriki, Barnabas anatumizidwa kukaona okhulupilira. Anaona chisomo cha Mulungu paokhulupilira, m’malo mobwelera ku Yerusalemu kukanena momwe nayendera, Barnaras anakayitana Paulo kuti akalalikire kwa nthawi yoyamba. Anazindikira bvumbulutso la Paul pa Yesu khristu mwa munthu.
Nkosadadwisa kuti ndi ku Antiokeya komwe okhulupilira anatchedwa akhristu.(Machitidwe11) “undifunse ndipo ndidzakupatsa amitundu akhale cholowa chako ndi malekedzero a dziko la pansi akhale ako ako”!(masalimo 2:7,8) chisilidziro cha mtanda ndicho kuti malekezero a dziko lapansi adzakumbukira ndikumbukira ndikubwelera kwa Ambuye(Masalimo 22:27)
“Ndilalira Yesu khristu monga mwa chinsinsi cha bvumbulutso lomwe linali lobisika kwa nthawi ya italic koma tsopano laulika poyera moonekera mwa uneneri mwwu a Mulungu”.
“Koma iye analisidwa chifukwa cha mphulupulu zanthu: chilango chititengera ife mtendere ife chinamugwera iye; ndipo ndi mikwngwilima yake ife tinachilisidwa”(Yesaya 53:4-5) Tsopano Mulungu wa muyaya analamulira kuti chinsinsichi chidzike kuti mafuko onse adziko lapansi azindikire za moyo omvera omwe umadza ndichinkhulupiliro”(Aroma:25,26)
“mapeto ake ndi akuti zinatenga tchito limodzi kuti munthu atsutsidwe, ndi kuchita kumodzi kwa chilungamo kunapanga munthu m’modzi kunapanga anthu ochimwa, kukhulupilika kwa munthu wina kunapanga anthu onse olungama(Aroma 5:18-19).
Chiphunzinso chachikhulupiliro ndicho kuona monga m’mene Mulungu aonera. Mulungu amayitana zinthu zimene kulibe ngati zilipo.(Aroma 4:17) “popeza sitipenyelera zinthu zogwirika koma tipeya mabvumbulutso osaoneka pa kalilore pamene paonekera khristu mwa munthu (2 Akolinto 3:18, 2 Akolinto 4:18).
Ahebri2;8 “Pakuti muja anangonjetsa zonse kwa iye,
Sanasiyepo kanthu kosamgonjera iye.koma
Sitinayamba tsopano apa kuona zonse zomgo
njera”.
Ahebri 2:9 Koma tiona wobvala korona wa ulemelero ndi
Ulemu kuti chisomo cha Mulungu alawe imfa
M’malo mwa munthu aliyense.
Ahebri 2:10 Pakuti kunamuyenera iye amane zonse ziri
Chifukwa cha iye, ndi zonse mwa iye,
Pakutenga ambiri alowe ulemelero, kum’konza
Wa mphumphu mtsogoleli woyamba wa
Chipulumutso chawo mwazowawa.
Ahebri 2:11 Pakuti iye wakuyeletsedwa achokera onse
Mwa m’modzi, chifukwa cha ichi alibe manyanzi
Kuwancha iwo Abale.
Mirror Translation Copyright Francois du Toit 2007. All Rights Reserved. Used by permission.Online Parallel Bible